Bwenzi Lanu
Yesu Bwenzi Lanu
Ndili ndi bwenzi. Iye ndi bwenzi loposa onse. Ndi woona ndi wokoma mtima kotero ndikadakonda mutam'dziwa Iye. Dzina lake ndi Yesu. Chinthu chosangalatsa ndi chakuti Iye akufuna kukhala bwenzi lanu.
Ntakuuzani za Iye. Nkhaniyi timawerenga m'Buku Lopatulika. Buku Lopatulika ndi loona. Ndi mau a Mulungu.
Mulungu ndi amene analenga dziko lapansi ndi zonse zokhala momwemo. Iye ndi Ambuye wakumwamba ndi dziko la pansi. Amapereka moyo ku zinthu zonse.
Nkhani yonse ya: Bwenzi Lanu
Yesu ndi mwana wa Mulungu. Mulungu anam'tumiza kuchokera kumwamba kubwera padziko lino lapansi kukhala Mpulumutsi wathu wathu.
Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero (kuthantauza kuti anatikonda inu ndi ine) kuti anapatsa Mwana wache wobadwa yekha, (kufera machimo athu) kuti yense wokhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha. (Yohane 3:16)
Yesu anabwera pa dziko lino lapansi monga mwana wakhanda. Abambo ndi amayi ake adziko lapansi anali Yosefe ndi Maria. Anabadwira m'khola la ng'ombe nagonekedwa m'chodyera ng'ombe.
Yesu anakula pamodzi ndi Yosefe ndi Maria ndipo Iye anali kumvera iwo. Iye anali ndi abale ocheza nawo. Ankathandiza Yosefe kupala matabwa.
Pamene Yesu atakula, anaphunzitsa anthu za Atate wake wakumwamba. Iye adawaonetsera kuti Mulungu ankawakonda. Ankachiza odwala ndi kutonthoza ovutika. Anali bwenzi la ana. Ankafuna ana akhale chifupi naye. Ana anali kumukonda Yesu ndipo anali kukonda kukhala naye pamodzi.
Anthu ena sankam'konda Yesu. Iwo anali kum'chitira nsanje ndipo kumuda. Ankamuda kwambiri moti anali kufuna kumupha. Linabwera tsiku losautsa, anamupha Yesu pomukhomera pa mtanda. Yesu sadalakwitse konse. Iye anatifera ife chifukwa cha zolakwa zathu.
Nkhani ya Yesu sikuthera pa imfa yake. Mulungu adamuukitsa Iye kwa akufa. Ophunzira ake adamuona Iye. Ndipo tsiku lina Iye anabwerera kumwamba. Lero akhoza kupenya ndi kumvera inu. Amadziwa zonse zokhudza inu ndipo amakusamalira. Mungobwera kwa Iye kudzera mu pemphero. Muuzeni zonse zokhudza nkhawa zanu. Ali wokonzeka kukuthandizani. Mutha kuweramitsa mutu wanu ndi kulankhula naye nthawi iliyonse, pena paliponse.
Tsiku lina Iye alinkubweranso. Adzatenga onse okhulupirira Iye kupita nao kwao kumwamba.