Nkhani yonse ya: Masiku Awiri Mu Gehena
Wandende mnzake wa Lenokisi adandiuza chinthu cha chilendo chomwe chidam'chitikira pa nthawi yomwe adali ngati wakufa. Nkhaniyi idandichititsa chidwi moti ndidafunitsitsa kukomana naye Lenokisi kuti ndimve nkhaniyi kuchokera pakamwa pake. Mwayi woti ndikomane naye sudapatsidwe kwa ine kwa miyezi ingapo, koma kenaka ndidakomana naye. Nditachotsedwa pantchito ya mu'mgodi ndidapatsidwa ntchito yolemba malipoti ena kuofesi ina yakundende. Tsiku lina nkhani yakuuka kwa akufa kwa munthu uja idakambidwa, nthawi yomweyo adadutsa pakhomo paofesi, ndipo adandilozera kwa iye. Posakhalitsa ndidam'patsa kalata yoti afike kumene ndidali kugwira ntchito. Atafika, ndidali ndi nthawi yokambirana naye, ndipo kuchokera pakamwa pake ndidamva nkhani yake yodabwitsa. Adali wachinyamata wosapyolera zaka makumi atatu, koma anakhwima m'makhalidwe a umbava. Adali munthu wophunzira bwino komanso wanzeru.
Mbali yodabwitsa ya nkhani yake idachitika panthawi imene adali wakufa. Popeza ndidali wotola nkhani mwachidule, ndidali kulemba zonse zomwe adali kundiuza.
Iye adati: “ Kuyambira m'mawa wonse ndidali nditadziwa kuti kanthu kena koopsya kadzachitika. Chifukwa cha nkhawa imeneyi ndidapita kwa woyang'anira wamkulu wa mumgodi, Bambo Grason, kuti ndimulongosolere momwe ndidali kumvera. Ndidam'pempha kuti adzaone malo omwe ndidali kugwirapo ntchito yokumba malasha. Adabwera, nakhala ngati wapimadi malowo, nandilamula kuti ndiyenera kupitiriza kugwira ntchito. Adandiuza kuti palibe choopsa chili chonse, naganiza kuti mutu wanga wasokonekera. Ine ndidabwerera ku ntchito yanga, ndipo ndidali kukumba kwa ntahwi yochepa, pamenepo ndidaona mwadzidzi kunali mdima waukulu. Kenaka padaoneka ngati chitseko chachitsulo chachikulu chidatseguka, ndipo ndidalowa pa khomo lake. Pamenepo ndidadziwa m'moyo mwanga kuti ndidali wakufa ndipo ndidali m'dziko lachilendo. Sindidathe kuona munthu wina ali yense kapena kumva china chilichonse, ayi. Mphamvu ina yosadziwika kwa ine idandiyendetsa kuchoka pakhomopo ndipo ndidayenda patali kufika m'mphepete mwa mtsinje waukulu. Kudali ngati usiku pamene pali nyenyezi zambiri, sikudali kowala kweni-kweni kapena mdima. Sipadapite nthawi yaitali, ndili kutsidya la mtsinjewo, ndidamva phokoso lotakasidwa madzi popalasa bwato. Posachedwa munthu amene adali m'bwatomo adapalasira kufika pafupi ndi pomwe ndidaima.
“ Nthawi imeneyo ndidali wopanda mawu. Iye adandiyang'ana kamphindi kochepa, nati kwa ine, 'ndabwera kudzakutenga,' nandiuza kuti tikwere bwatolo kuti tiolokere tsidya lina. Ndidamumvera. Padalibe mawu ena amene adalankhulidwa. Ndidali kufuna kuti ndimufunse dzina lake ndiponso kumene ndili, koma sindidathe chifukwa lilime langa lidamamatira m'kamwa mwanga, kotero kuti sindidathe kunena liwu lililonse. Kenaka tidafika tsidya lina la mtsinjewo ndipo ndidachoka m'bwatomo. Nditaturukamo wopalasa bwato uja anandikanganukira kumaso kwanga, nandichokera.
“Atandisiya choncho, ndidasowa chochita. Poyang’ana patsogolo panga, ndidaona njira ziwiri zidaloza ku chigwa cha mdima. Njira imodzi idali yotambalala imene imaoneka kuti ndi yotakata. Njira ina idali yopapatiza yopita mbali ina, koma ine ndidatsata njira yaikulu yotakata ija. Sindidapite patali pamene ndidaona kuchuluka kwa mdima udali nkukulabe. Komabe ndidali kuona kuwala kochokera patali, potero ndidaunikiridwa pa ulendo wangawo.
“Posachedwa ndidakomana ndi chinthu china, maonekedwe ake sindingathe kulongosola, koma ndingalongosole pang’ono maonekedwe ake oopsya. Maonekedwe ake adali ngati munthu, koma adali wamkulu koposa munthu aliyense amene ndidamuonapo. Utali wake udali monga ngati mamita atatu. Adali ndi mapiko akulu kumbuyo kwake. Adali wakuda monga ngati malasha omwe ndinali kukumba. Adali wamaliseche wosavala chirichonse. M’dzanja lake adagwira nthungo yotalika pafupifupi mamita asanu. Maso ake adawala ngati mipira ya moto. Mano ake adali oyera kwambiri ndipo utali wake monga ngati inchi imodzi. Mphuno yake idali yaikulu ndithu yotambalala yokhala yophwaphwatika. Tsitsi lake lidali lokhakhala, losaoneka bwino, lalitali, ndipo linagwera m’mapewa ake akulu. Mawu ake anabangula monga mau a mkango.
“Idali nthawi yowala mu mdimamo imene ndidamuona poyamba. Ine ndidanjenjemera kwambiri monga tsamba la mtengo logwedezeka ndi mphepo. Adakweza nthungo m’dzanja lake kuloza kwa ine nakhala ngati afuna kundiponyera. Mwadzidzidzi ndidaima. Ndili wonjenjemera chomwecho, adanena ndi mawu woopsya amene ndikuwakumbukirabe, nandiuza kuti ndimutsate iye chifukwa watumidwa kuti anditsogolere pa ulendo wangawo. Ndipo ndidamutsata. Ndi chiyani chomwe ndikadachita? Titayenda patali pang’ono, phiri lalikulu lidaonekera patsogolo pathu. Lidaoneka phiri longa logawidwa pakati, ndipo pa mbali ina ya phirilo inali khoma lalitali. Pakhomapo padali mau olembedwa: ’MALO A GEHENA’. Wonditsogolera adafika pakhoma la phirilo nagogoda katatu ndi chogwirira cha nthungo yake. Ndipo chitseko chachikulu chidatseguka cham’tsogolo, ndipo tidalowa mkati. Pamenepo adanditsogolera kupyolera mkati mwa phirilo.
“Pa kanthawi tidayenda mumdima waukulu. Ndidali kumva mgugu wa mapazi oyenda kotero kuti ndidatha kutsatira wonditsogolerayo. M’njira yonseyo ndinali kumva kubuula monga ngati wina alinkufa. Popitirira ndi ulendo wathu kuliraku kudali kuchuluka, ndipo onsewo adali kulira poitanitsa, ‘Madzi, madzi, madzi.’ Tsopano titafika pakhomo lina, popitirira, ndidamva mau wolira mochuluka ngati anthu okwana zikwi chikwi patali. Ndipo kulirako kudalinso kupempha, ‘Madzi, madzi, madzi.’ Posachedwa khomo lina lalikulu lidatseguka wonditsogolera atagogoda. Ndidapeza kuti tidayenda mopyola mkati mwa phiri lija, ndipo ndidaona chigwa chachikulu chili patsogolo panga.
“Pamalo amenewa wonditsogolerayo adandisiya ndekha, napita kukatsogoleranso mizimu ya anthu ena otayika kunjira yomwe tidadzerayo. Ndidakhala pa chigwa chotsegukacho kanthawi pamene munthu wina wokhala ngati woyamba uja adabwera kwa ine; koma m’malo mokhala ndi nthungo, iye adabwera ndi lupanga lalikulu. Iye adabwera kudzandiuza za chionongeko changa cham’tsogolo. Adalankhula ndi mau oopsya amene adakhudza moyo wanga. Adati, ‘Iwe, uli ku Gehena. Chiyembekezo chako chonse chathawa. Pobwera kuno udayenda kupyola m’phirimo, ndipo udali kumva kulira kwa anthu otayikawo, amene adali kupempha madzi kuti athe kuziziritsa malilime awo otenthedwa. Panjira imeneyo pali khomo lolowera kupita ku nyanja ya moto. Posachedwa kumeneko kudzakhala chionongeko chako. Musanaperekezedwe ku malo amazunzo awo, kumene simudzatulukanso (chifukwa kulibenso chiyembekezo kwa amene alowamo) mudzaloledwa kuima malo achigwa ngati ano, kumene kwapatsidwa kwa onse otaika, kuonetsedwa zabwino zomwe akanazilandira, koma m’malo mwake alinkulandira chilango.
“Zitatha izi ndidapezeka ndiri ndekha. Kapena chifukwa cha kuopsedwa kwambiri pa njira, sindikudziwa, koma tsopano ndidapezeka wolefuka. Kufooka ndi kusamva kudagwira thupi langa, mphamvu zanga zidachoka, ziwalo zanga zidalephera kulimbitsa thupi langa. Ndidathedwa, ndipo ndidagwa pansi. Ndidakhala ngati ndakomoka, monga munthu wogona koma ali ndi moyo, ndipo ndidaona ngati ndikulota. Poyang’ana kumwamba patali ndi ine, ndidapenya mzinda wokongola ndithu womwe timauwerenga m’Buku Lopatulika. Makoma ake adanyezimira ngati miyala ya yaspi ndipo pambali pa mzindawo ndidaona malo akulu okutidwa ndi maluwa okongola kwambiri. Ndidaonanso mtsinje wa moyo ndi nyanja yowala ngati galasi. Ndipo angelo ochuluka adali kulowa ndi kutuluka pa zipata za mzindawo, ali kuimba nyimbo zokoma. Pakati pawo ndidaona mayi wanga wokondedwa amene adafa zaka zapitazo ndi mtima wawo wosweka chifukwa cha zoipa zomwe ndidali kuchita. Mayi adandiyang’ana nandikodola kuti ndipite komwe kudali iwo. Koma ine sindidathe kusuntha pomwe ndidali. Kudaoneka ngati ndili ndi chinthu cholemera kwambiri chomwe chidandikanikiza pansi. Pamenepo mphepo yabwino idawomba kuloza kwa ine ndi kununkhira kochokera m’maluwa okongola aja kudandifikira ine. Ndidamva kuyimba kokoma kwa angelo, ndipo ine ndidalira ndi kunena, ‘Ndikadakhala m’modzi wa iwo.’
“Ndidakali kumwera chikho chokomachi poona zokoma zonse, mwadzidzidzi chidachotsedwa kukamwa kwanga. Munthu uja anandidzutsa kutulo tanga, ndipo nandichotsa ku dziko labwino lomwe ndidali kuona masomphenya. Anandiuza kuti, ‘Ndi nthawi tsopano yokalowa komwe iwe udzakhala. Munditsate ine.’ Pamene ndidayamba kuyenda, ndidalowanso munjira ya mdima. Ndidamtsatira wonditsogolera kanthawi, pamene tinafika pakhomo lotseguka pambali. Popitirira pamenepo tidapezeka tili kulowa pakhomo pena, ndipo taonani ndidaona nyanja ya moto! Nditapenya polekezera maso anga ndidaonadi nyanja ya moto ndi miyala ya moto. Mafunde akulu a moto adali kukweranakwerana, funde lina pa linzake. Malawi a moto adali kukwera m’mwamba monga mafunde a m’nyanja owinduka ndi mphepo yaikulu. Ndidapenya anthu alikulimbana ndi mafunde a motowo, koma mafundewo adali kuwakanikiza pansi pakuya munyanja ya moto. Pamwamba pa mafunde akulu a moto padaoneka anthu, kwa kanthawi adali kutukwana moipitsitsa Mulungu wolungamayo. Kulira kwao kolilira madzi kudali komvetsa chisoni. M’nyanja yamoto imeneyi mudali kumveka mau olira ndi kulira kosalekeza kuchokera ku mizimu yotaikayo.
“Pamenepo ndidatembenuza maso anga kuyang’ana pakhomo pamene ndidalowapo posachedwa, ndipo ndidawerenga mau olembedwa motere: ‘MALO ANO NDI A CHILANGO CHAKO, KUNTHAWI YOSATHA.’ Posakhalitsa ndidaona nthaka ilikuchoka ku mapazi anga, pomwepo ndidapezeka ndili kumira munyanja yamoto. Ludzu losaneneka lofuna madzi lidabwera kwa ine. Ndili kuitanitsa madzi, maso anga adatseguka, ndipo ndidapeza kuti ndili ku chipatala cha kundende.
“Sindidauze aliyense nkhani imeneyi kale lonse, chifukwa ndidali kuchita mantha kuti akulu oyang’anira m’ndende akadandiganizira kuti ndazungulira mutu, ndi kundisekera m’chipatala cha amisala. Ine ndidapyola mu zonsezi, ndipo ndili wokhutitsidwa kuti Kumwamba kulipo, Gehena ilipo, ndi Gehena yakaleyo imene Buku Lopatulika limanena nthawi zonse. Koma choonadi ndi ichi, ine sindidzapitanso ku malo a Gehenawo ayi.
“Pamene ndidatsegula maso anga mu chipatala ndi kuona kuti ndili ndi moyonso mdziko lino, nthawi yomweyo ndidapereka mtima wanga kwa Mulungu, ndipo ndidzakhalabe Mkhristu mpaka imfa. Sindidzaiwala konse kuopsa kwa Gehena ndi zokoma zakumwamba zomwe ndidaziona. Ine ndakonzeka kukakomana ndi wokondedwa mayi anga omwe ali kale komweko. Ndipo ndidzaloledwa kukhala pansi pa m’mbali mwa mtsinje wokongolawo, ndipo ndidzatha kuyenda ndi angelowo kuwoloka chigwacho ndi kupyola mapiri omwe akutidwa ndi kununkhira kwa maluwa omwe kukongola kwake kosayerekeza ndi kanthu kalikonse ka m’dziko lino lapansi. Ndidzakhala ndikumvera nyimbo za anthu owomboledwa. Panopa ndasiya zokondweretsa za dziko zomwe ndidayendamo kale ndisadabwere ku ndende, chifukwa zokoma za Kumwamba zidzaposa zonsezo. Ndawasiyanso abwenzi omwe ndidali kuchita nawo zoipa, ndiyenera kugwirizana ndi anthu a makhalidwe abwino ndikadzatuluka mundende.”
Tikupereka nkhani imeneyi kwa awerengi onse monga momwe ife tidailandira ndi kuimva kuchokera kwa Bambo Lenokisi mwini wake. Mulungu wamphamvu yonse adalitse uthenga umenewu kuti uthe kutsitsimutsa mizimu ya anthu otaika kuti apeze chipulumutso.
Ha! Kodi anthu angakayike bwanji kuti kuli Gehena? Tili ndi Buku Lopatulika ndilo mau a Mulungu ndiponso mabvumbulutso monga a Bambo Lenokisi amene aphunzitsa za Gehena. Abambo ndi amai, khalani chete! Choonadi chilipo! Moyo wanu udzawerengedwa! Mulungu akufuna kukupulumutsani, ndipo adzaku-khululukirani ngati muvomereza kuti ndinu wochimwa. Njira yokhayo yoloza kuchipulumutso ndi kutsukidwa kuchokera ku machimo pakuvomereza mwazi wa Yesu Kristu monga nsembe ku machimo anu. Mukalandira chikhululukirochi kuchokera kwa Mulungu, Adzakupatsani mtendere ndi mpumulo m’mtima mwanu. Mungakhale womasuka m’moyo uno, komanso wokonzeka kulandira chisangalalo cha kumwamba m’malo mwa ku khala ku Gehena osati masiku awiri okha koma m’paka muyaya.
Fanizo la mwini Cuma ndi Lazaro waumphawi
Luka 16:19-31
“Ndipo panali munthu mwini cuma amabvala cibakuwa ndi nsaru yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse; ndipo wopempha-pempha wina, dzina lake Lazaro, adaikidwa pakhomo pace wodzala ndi zironda, ndipo anafuna kukhuta ndi zakugwa pa gome la mwini cumayo; komatu agarunso anadza nanyambita zironda zace. Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti adatnegedwa iye ndi angelo kunka ku cifuwa ca Abrahamu; ndipo mwini cumayo adfanso, naikidwa m’manda.
“Ndipo m’Hade anakweza maso ace, pokhala nao mazunzo, naona Abrahamu patali, ndi Lazaro m’cifuwa mwace. Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundicitire cifundo, mutume Lazaro, kuti abviike nsonga ya cala cace m’madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m’lawi ili la moto. Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukila kuti unalandira zokoma zako pakukhala m’moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi. Ndipo pamwamba pa izi, pakati pa ife ndi inu pakhazikika phompho lalikuru, kotero kuti iwo akufuna kuoloka kucokera kuno kunka kwa inu sangathe, kapena kucokera kwanuko kuyambuka kudza kwa ife, sangathenso. Koma anati, Pamenepo ndiku-pemphani, Atate, kuti mumtume ku nyumba ya atate wanga; pakuti ndiri nao abale asanu; awacitire umboni iwo kuti iwonso angadze ku malo ano a mazunzo. Koma Abrahamu anati, Ali ndi Mose ndi aneneri; amvere iwo. Koma anati, Iai, Atate Abrahamu, komatu ngati wina akapita kwa iwo wocokera kwa akufa adzasandulika mtima. Koma anati kwa iye, Ngati samvera Mose ndi aneneri, sadzakopeka mtima ngakhale wina akauka kwa akufa.
Malemba ena: Cibvumbulutso 21:7-8, Cibvumbulutso 20:10,12,13; 2 Petro 3:10-12.
Lumikizanani nafe.
Pezani mauthenga olembedwa.